Psalms 142

Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.

1Ndikulirira Yehova mofuwula;
ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.
2Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;
ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

3Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,
ndinu amene mudziwa njira yanga.
Mʼnjira imene ndimayendamo
anthu anditchera msampha mobisa.
4Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;
palibe amene akukhudzika nane.
Ndilibe pothawira;
palibe amene amasamala za moyo wanga.

5Ndilirira Inu Yehova;
ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,
gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”
6Mverani kulira kwanga
pakuti ndathedwa nzeru;
pulumutseni kwa amene akundithamangitsa
pakuti ndi amphamvu kuposa ine.
7Tulutseni mʼndende yanga
kuti nditamande dzina lanu.

Ndipo anthu olungama adzandizungulira
chifukwa cha zabwino zanu pa ine.
Copyright information for NyaCCL